Tiago 2

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (NYA) vs VC

Sair da comparação
VC Versão Católica
1 Abale anga, okhulupirira Yesu Khristu waulemerero, musaonetse tsankho.
1 Meus irmãos, na vossa fé em nosso glorioso Senhor Jesus Cristo, guardai-vos de toda consideração de pessoas.
2 Tangoganizirani, pakati panu patabwera munthu atavala mphete yagolide ndi zovala zapamwamba, ndipo winanso wosauka nʼkulowa atavala sanza.
2 Suponde que entre na vossa reunião um homem com anel de ouro e ricos trajes, e entre também um pobre com trajes gastos;
3 Ngati musamala kwambiri munthu wovala bwinoyu uja, nʼkumuwuza kuti, “Khalani pa mpando wabwinowu,” koma wosauka uja nʼkumuwuza kuti, “Ima apo,” kapena “Khala pansi pafupi ndi chopondapo mapazi angawa,”
3 se atenderdes ao que está magnificamente trajado, e lhe disserdes: Senta-te aqui, neste lugar de honra, e disserdes ao pobre: Fica ali de pé, ou: Senta-te aqui junto ao estrado dos meus pés,
4 kodi simunachite tsankho pakati panu ndi kukhala oweruza a maganizo oyipa?
4 não é verdade que fazeis distinção entre vós, e que sois juízes de pensamentos iníquos?
5 Tamverani abale anga okondedwa, kodi Mulungu sanasankhe amene dziko lapansi limawaona ngati amphawi kuti akhale olemera mʼchikhulupiriro ndi kulowa ufumu umene Iye analonjeza kwa amene amamukonda?
5 Ouvi, meus caríssimos irmãos: porventura não escolheu Deus os pobres deste mundo para que fossem ricos na fé e herdeiros do Reino prometido por Deus aos que o amam?
6 Koma mwakhala mukunyoza amphawi. Kodi si anthu olemerawa amene akukudyerani masuku pamutu? Si anthu amenewa amene amakukokerani ku bwalo la milandu?
6 Mas vós desprezastes o pobre! Não são porventura os ricos os que vos oprimem e vos arrastam aos tribunais?
7 Kodi si omwewa amene amachita chipongwe dzina la wolemekezeka, limene inu mumatchulidwa?
7 Não blasfemam eles o belo nome que trazeis?
8 Ngati musungadi lamulo laufumu lija lopezeka mʼMalemba lakuti, “Konda mnansi wako monga iwe mwini,” ndiye kuti mukuchita bwino.
8 Se cumprirdes a lei régia da Escritura: Amarás o teu próximo como a ti mesmo {Lv 19,18}, sem dúvida fazeis bem.
9 Koma mukamaonetsa tsankho mukuchimwa, ndipo ndinu wochimwa monga wophwanya lamulo.
9 Mas se vos deixais levar por distinção de pessoas, cometeis uma falta e sereis condenados pela lei como transgressores.
10 Pakuti amene amasunga Malamulo onse, akangophwanya fundo imodzi yokha, waphwanya Malamulo onse.
10 Pois quem guardar os preceitos da lei, mas faltar em um só ponto, tornar-se-á culpado de toda ela.
11 Pakuti amene anati “Usachite chigololo” ndi yemweyonso anati “Usaphe.” Ngati suchita chigololo koma umapha, ndiwe wophwanya Malamulo.
11 Porque aquele que disse: Não cometerás adultério, disse também: Não matarás {Ex 20,13s}. Se, pois, matares, embora não tenhas cometido adultério, tornas-te transgressor da lei.
12 Muziyankhula ndi kuchita zinthu monga anthu amene mudzaweruzidwe ndi lamulo limene limapereka ufulu,
12 Falai, pois, de tal modo e de tal modo procedei, como se estivésseis para ser julgados pela lei da liberdade.
13 chifukwa munthu woweruza mopanda chifundo, nayenso adzaweruzidwa mopanda chifundo. Chifundo chimapambana pa chiweruzo.
13 Haverá juízo sem misericórdia para aquele que não usou de misericórdia. A misericórdia triunfa sobre o julgamento.
14 Abale anga, phindu lake nʼchiyani ngati munthu anena kuti ali ndi chikhulupiriro koma chopanda ntchito zabwino? Kodi chikhulupiriro choterechi chingamupulumutse?
14 De que aproveitará, irmãos, a alguém dizer que tem fé, se não tiver obras? Acaso esta fé poderá salvá-lo?
15 Tangoganizirani, mʼbale kapena mlongo amene ali ndi usiwa, ndipo alibe chakudya cha tsiku ndi tsiku.
15 Se a um irmão ou a uma irmã faltarem roupas e o alimento cotidiano,
16 Ngati mmodzi wa inu amuwuza kuti, “Pita ndi mtendere, ukafundidwe ndipo ukakhute,” koma osamupatsa zimene akuzisowa, phindu lake nʼchiyani pamenepa?
16 e algum de vós lhes disser: Ide em paz, aquecei-vos e fartai-vos, mas não lhes der o necessário para o corpo, de que lhes aproveitará?
17 Chomwechonso, chikhulupiriro chokha chopanda ntchito zabwino ndi chakufa.
17 Assim também a fé: se não tiver obras, é morta em si mesma.
18 Koma wina anganene kuti, “Inuyo muli ndi chikhulupiriro koma ine ndili ndi ntchito zabwino.”
18 Mas alguém dirá: Tu tens fé, e eu tenho obras. Mostra-me a tua fé sem obras e eu te mostrarei a minha fé pelas minhas obras.
19 Mumakhulupirira kuti kuli Mulungu mmodzi yekha. Mumachita bwino. Komatu ngakhale ziwanda zimakhulupirira zimenezi ndipo zimanjenjemera ndi mantha.
19 Crês que há um só Deus. Fazes bem. Também os demônios crêem e tremem.
20 Munthu wopusa iwe, kodi ukufuna umboni woti chikhulupiriro chopanda ntchito zabwino nʼchakufa?
20 Queres ver, ó homem vão, como a fé sem obras é estéril?
21 Kodi Abrahamu kholo lathu sanatengedwe kukhala wolungama chifukwa cha zimene anachita pamene anapereka mwana wake Isake pa guwa lansembe?
21 Abraão, nosso pai, não foi justificado pelas obras, oferecendo o seu filho Isaac sobre o altar?
22 Tsono mukuona kuti chikhulupiriro chake ndi ntchito zabwino zinkachitika pamodzi, ndipo chikhulupiriro chake chinasanduka chenicheni chifukwa cha ntchito zake zabwino.
22 Vês como a fé cooperava com as suas obras e era completada por elas.
23 Ndipo Malemba akunena kuti, “Abrahamu anakhulupirira Mulungu ndipo anatengedwa kukhala wolungama,” ndipo anatchedwa bwenzi la Mulungu.
23 Assim se cumpriu a Escritura, que diz: Abraão creu em Deus e isto lhe foi tido em conta de justiça, e foi chamado amigo de Deus {Gn 15,6}.
24 Tsono mukuona kuti munthu amasanduka wolungama ndi ntchito zabwino osati ndi chikhulupiriro chokha ayi.
24 Vedes como o homem é justificado pelas obras e não somente pela fé?
25 Nʼchimodzimodzinso, kodi wadama uja, Rahabe, sanasanduke wolungama chifukwa cha zomwe anachita pamene anapereka malo ogona kwa azondi aja ndi kuwathawitsira mbali ina?
25 Do mesmo modo Raab, a meretriz, não foi ela justificada pelas obras, por ter recebido os mensageiros e os ter feito sair por outro caminho?
26 Monga thupi lopanda mzimu ndi lakufa, chomwechonso chikhulupiriro chopanda ntchito zabwino ndi chakufa.
26 Assim como o corpo sem a alma é morto, assim também a fé sem obras é morta.

Ler em outra tradução

Comparar com outra

Estude este capítulo no WhatsApp

Peça à IA da Bíblia Fala para explicar Tiago 2, comparar traduções ou montar um estudo — tudo direto pelo WhatsApp.