Isaías 20

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (NYA)

1 Mʼchaka chimene mkulu wankhondo wotumidwa ndi mfumu ya ku Asiriya, anabwera ku Asidodi ndi kuwuthira nkhondo ndi kuwulanda,

2 nthawi imeneyo Yehova anawuza Yesaya mwana wa Amozi kuti, “Pita kavule chiguduli ndi nsapato zako.” Ndipo iye anaterodi, ankangoyenda wamaliseche ndiponso wopanda nsapato.

3 Kenaka Yehova anati, “Monga momwe mtumiki wanga Yesaya wakhala akuyendera wamaliseche ndiponso wopanda nsapato kwa zaka zitatu ngati chizindikiro ndi chenjezo kwa dziko la Igupto ndi Kusi,

4 momwemonso mfumu ya ku Asiriya idzatenga ukapolo anthu a ku Igupto ndi a ku Kusi, anyamata ndi okalamba. Iwo adzakhala amaliseche ndi opanda nsapato, matako ali pa mtunda. Zimenezi zidzachititsa manyazi Igupto.

5 Amene ankadalira Kusi, ndiponso amene ankadzitukumula chifukwa cha Igupto adzakhumudwa ndi kuchita manyazi.

6 Tsiku limenelo anthu amene amakhala mʼmbali mwa nyanja adzati, ‘Taonani zomwe zawachitikira amene ife tinkawadalira, amene ife tinkathawirako kuti atithandize ndi kutipulumutsa kwa mfumu ya ku Asiriya! Nanga ife tidzapulumuka bwanji?’ ”

Ler em outra tradução

Comparar lado a lado

Estude este capítulo no WhatsApp

Peça à IA da Bíblia Fala para explicar Isaías 20, comparar traduções ou montar um estudo — tudo direto pelo WhatsApp.